Jeremiah 48

Uthenga Wonena za Mowabu

1Ponena za Mowabu:

Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti,

“Tsoka kwa mzinda wa Nebo, chifukwa wawonongedwa.
Mzinda wa Kiriyataimu wachititsidwa manyazi ndipo wagonjetsedwa;
linga lichititsidwa manyazi ndipo lagumulidwa.
2Palibenso amene akutamanda Mowabu;
ku Hesiboni anthu anamupanganira zoyipa:
‘Bwerani, tiyeni timuwonongeretu kuti asakhalenso mtundu wa anthu.’
Inunso anthu a ku Madimena, adzakukhalitsani chete;
ankhondo adzakupirikitsani.
3Tamvani mfuwu wa anthu a ku Horonaimu.
Iwo akulira kuti, ‘Kusakazika ndi kuwonongeka kwakukulu.’
4Mowabu wawonongeka;
ana ake angʼonoangʼono akulira kwambiri.
5Anthu akukwera chikweza cha ku Luhiti,
akulira kwambiri pamene akupita.
Kulira chifukwa cha chiwonongeko kukumveka
pa njira yotsikira ku Horonaimu.
6Thawani! Dzipulumutseni;
khalani ngati mbidzi ya mʼchipululu.
7Popeza inu munkadalira ntchito zanu ndi chuma chanu,
nanunso mudzatengedwa ukapolo,
ndipo Kemosi adzapita ku ukapolo,
pamodzi ndi ansembe ake ndi akuluakulu ake.
8Wowononga adzabwera ndi kusakaza mzinda uliwonse,
ndipo palibe mzinda umene udzapulumuke.
Chigwa chidzasanduka bwinja
ndipo malo athyathyathya a pamwamba pa phiri adzawonongedwa
monga Yehova wayankhulira.
9Mtsineni khutu Mowabu
chifukwa adzasakazika;
mizinda yake idzasanduka mabwinja,
wopanda munthu wokhalamo.

10“Wotembereredwa munthu amene amagwira ntchito ya Yehova monyinyirika!
Wotembereredwa munthu amene amaletsa lupanga lake kupha anthu!

11“Mowabu wakhala pa mtendere kuyambira ubwana wake,
ngati vinyo wokhazikika pa masese ake,
osapungulidwa kuchoka mu mtsuko wina kuthira mu mtsuko wina;
iye sanatengedwepo ukapolo.
Nʼchifukwa chake kukoma kwake nʼkomwe kuja
ndipo fungo lake silinasinthe.
12Nʼchifukwa chake masiku akubwera,”
akutero Yehova,
“pamene ndidzatuma anthu amene amakhuthula vinyo mʼmitsuko
ndipo adzamukhutula;
adzakhuthula vinyo yense mitsuko yake
pambuyo pake nʼkuphwanya mitsukoyo.
13Pamenepo Mowabu adzachita manyazi ndi Kemosi,
monga momwe Aisraeli anachitira manyazi
ndi Beteli amene ankamukhutulira.

14“Kodi munganene bwanji kuti, ‘Ife ndife asilikali.
Ife ndife ngwazi, anthu amphamvu pa nkhondo?’
15Owononga Mowabu ndi mizinda yake abwera ndipo ankhondo adzalowa mʼmidzi yake;
anyamata ake okongola apita kukaphedwa,”
ikutero Mfumu, imene dzina lake ndi Yehova Wamphamvuzonse.
16Kugwa kwa Mowabu kuli pafupi;
masautso ake akubwera posachedwa.
17Mulireni kwambiri, inu nonse amene mwamuzungulira,
inu nonse amene mumadziwa za kutchuka kwake;
nenani kuti, “Taonani momwe yathyokera ndodo yamphamvu yaufumu ija,
taonani momwe ndodo yaulemu yathyokera!”

18“Tsikani pa ulemerero wanu
ndipo khalani pansi powuma,
inu anthu okhala ku Diboni,
pakuti wowononga Mowabu
wabwera kudzamenyana nanu,
wasakaza mizinda yanu yotetezedwa.
19Inu amene mumakhala ku Aroeri,
imani mʼmbali mwa msewu ndi kumaonerera.
Funsani mwamuna amene akuthawa ndiponso mkazi amene wapulumuka,
afunseni kuti, ‘Kodi chachitika nʼchiyani?’ ”
20Iwo adzayankha kuti, “Mowabu wachititsidwa manyazi, pakuti wasakazika.
Lirani mwachisoni ndipo fuwulani!
Lengezani ku mtsinje wa Arinoni
kuti Mowabu wawonongedwa.
21Chiweruzo chabwera ku mizinda ya ku mapiri,
ndiyo Holoni, Yaza, Mefaati,
22Diboni, Nebo, Beti-Dibilataimu,
23Kiriyataimu, Beti-Gamuli, Beti-Meoni,
24Keriyoti ndi Bozira
ndi mizinda yonse ya Mowabu, yakutali ndi yapafupi yomwe.
25Mphamvu za Mowabu zawonongeka;
mkono wake wathyoka,”
akutero Yehova.

26“Muledzeretseni Mowabu,
chifukwa anadzikuza powukira Yehova.
Mulekeni Mowabu avivinizike mʼmasanzi ake;
mulekeni akhale chinthu chomachiseka.
27Kodi suja Israeli anali kwa iwe ngati chinthu chomachiseka?
Kodi Israeli anapezeka pakati pa akuba
kuti nthawi zonse poyankhula za iye,
iwe uzimupukusira mutu momunyoza?
28Inu amene mumakhala ku Mowabu,
siyani mizinda yanu ndi kukakhala pakati pa matanthwe.
Khalani ngati nkhunda imene imamanga chisa chake
pa khomo la phanga.

29“Tamva za kunyada kwa Mowabu,
kunyada kwake nʼkwakukulu.
Ndi wodzitama, wonyada ndi wodzitukumula.
Ali ndi mtima wodzikweza.
30Ine ndikuzidziwa ntchito zake,
akutero Yehova.
Ntchitozo ndi nʼzosapindulitsa kanthu.
31Nʼchifukwa chake ndidzamulira Mowabu,
ine ndikulira chifukwa cha anthu onse a ku Mowabu,
ndikubuwula chifukwa cha anthu a ku Kiri Heresi.
32Ndikukhetsa misozi chifukwa cha inu, kupambana momwe ndinalirira Yazeri.
Inu anthu a ku Sibina muli ngati mipesa
imene nthambi zake zatambalala mpaka ku Nyanja;
zafika mpaka ku nyanja ya Yazeri.
Wowononga wasakaza
zipatso zake zachilimwe ndi mpesa.
33Chimwemwe ndi chisangalalo zatha
ku minda ya zipatso ya ku Mowabu.
Ndaletsa kuchucha kwa vinyo mopsinyira mphesa;
palibe amene akufuwula mokondwa akamapsinya mphesa.
Ngakhale kufuwula kulipo,
koma sikufuwula kwa chimwemwe.

34“A ku Hesiboni ndi Eleali akulira
ndipo mfuwu wawo ukumveka mpaka ku Yahazi,
kuchokera ku Zowari mpaka ku Horonaimu ndi ku Egilati Selisiya.
Ngakhale madzi a ku Nimurimu aphwa.
35Ndidzawaletsa anthu a ku Mowabu
kupereka nsembe mʼmalo awo opembedzera
ndi kufukiza lubani kwa milungu yawo,”
akutero Yehova.
36“Nʼchifukwa chake mtima wanga ukulirira Mowabu ngati chitoliro.
Mtima wanga ukulirira anthu a ku Kiri Heresi ngati chitoliro
chifukwa chuma chimene anachipata chatha.
37Aliyense wameta mutu wake
ndi ndevu zake;
manja a munthu aliyense ndi ochekacheka,
ndipo munthu aliyense wavala chiguduli mʼchiwuno mwake.
38Pa madenga onse a ku Mowabu
ndiponso mʼmisewu yake
anthu akungolira,
pakuti ndaphwanya Mowabu
ngati mtsuko wopanda ntchito,”
akutero Yehova.
39“Taonani mmene waphwanyikira! Tamvani momwe akulirira!
Taonani momwe Mowabu wachititsidwira manyazi.
Mowabu wasanduka chinthu chonyozeka,
chinthu chochititsa mantha kwa onse amene amuzungulira.”
40Yehova akuti,

“Mtundu wina udzachita kuwuluka nʼkugwera pa Mowabu ngati chiwombankhanga
chimene chatambalitsa mapiko ake.
41Mizinda idzagwidwa
ndipo malinga adzalandidwa.
Pa tsiku limenelo mitima ya ankhondo a ku Mowabu
idzakhala ngati mtima wa mayi pa nthawi yake yochira.
42Mowabu sudzakhala mtundu wa anthu
chifukwa unadzikuza powukira Yehova.
43Zoopsa, dzenje ndi msampha zikudikira
inu anthu a ku Mowabu,”
akutero Yehova.
44“Aliyense wothawa zoopsa
adzagwera mʼdzenje,
aliyense wotuluka mʼdzenje
adzakodwa mu msampha.
Ndigwetsa zimenezi pa Mowabu
pa nthawi ya chilango chake,”
akutero Yehova.

45“Anthu othawa nkhondo ayima pa mthunzi wa Hesiboni
chifukwa chotopa.
Koma moto wayaka kuchokera ku Hesiboni,
malawi a moto abuka kuchokera ku nyumba ya mfumu Sihoni.
Motowo ukuwononga mapiri a ku Mowabu,
dziko la anthu onyada.
46Tsoka kwa iwe Mowabu!
Anthu opembedza Kemosi awonongeka.
Ana ako aamuna ndi aakazi
atengedwa ukapolo.

47“Komabe masiku akutsogolo
ndidzabwezeranso Mowabu chuma chake,”
akutero Yehova.
Chiweruzo cha Mowabu chathera pamenepa.

Copyright information for NyaCCL